Njira Yopachikidwa


Ine ndikufuna ndikufunseni funso, ngati ndinu Mkhristu. Kodi munayamba mwadabwapo chifukwa chimene kuyambira pamene munadzakhala Mkhristu, kuti mukumakhala ndi mavuto ochuluka ndi zosautsa kuposa kale? Chabwino chiripo chifukwa chake. Poyamba pa zonse, ndi chifukwa cha kuti inu mwasanduka mdani wa chosalungama cha Satana. Inu mwaiyamba nkhondo. Chifukwa china ndi chakuti, inu musanakhale mwana wa Mulungu, inu munkhala wopanda kukwapulidwa ndi kukonzedwa. Timakwapulidwa ndi Mulungu, monga bambo angamukonzere mwana wake, kuti ife tisamaweruzidwe ndi dziko. Iye amatiuza ife tizidziweruza tokha; izo ndi zakuti, tizilingalira za njira zathu pamaso pa Mulungu mukuwala kwa Mawu Ake ndi njira, potero tidzathawa kukwapulidwa kochuluka, koma chifukwa ife timalephera kudziweruza tokha, ndiye tiziweruzidwa pamaso pa Mulungu.

Malemba amatiuza ife kuti machimo a anthu ena amatsogola kupita pa chiweruzo. Awa ndi machimo amene alapidwa, ndipo iwo amaweruzidwa mu chifundo. Machimo a anthu ena amawatsatira iwo osalapidwa ndipo amaweruzidwa mu mkwiyo pa chiweruzo.iye amene aphimba tchimo lake sadzachita bwino, koma aliyense wowulula machimo ake nawasiya iwo adzachita bwino (pezani chifundo). Kumbukirani, tchimo lirilonse liri pansi pa magazi kupatula tchimo limene liri lochitira dala, chomwe chikutanthauza kuti china chake chimene ukudziwa kuchita bwino kuti usachite. Magazi samaphimba tchimo ili, ndipo iwe uyenera kukwapulidwa ngati mwana wosamvera. Anthu ena amakwapulidwa kwambiri podutsa mmayesero otsatizana, ndipo potsiriza amapulumutsidwa ngati kupulumuka mu moto. Ntchito zawo zonse zimawotchedwa chifukwa ntchito zawo ndi zathupi, kutanthauza ntchito zoipa, zomwe sizinawapindulire iwo kapenanso Mulungu. Awa ataya gawo lalikulu la mphoto yawo, chotero tiyeni ife tisakhale monga iwo, koma tiyeni tizitenge ntchito zina limodzi nafe.

Njira ina yokhalira ndi mavuto ndi kupereka malo kwa Satana pongonyalanyaza moyo wodzikhuthula. Yesu anati tizipenyerera ndi kupemphera. Amayi ambiri samawayang’anira ana awo, pomaganiza kuti Mulungu awayang’anira iwo, koma bwenzi langa, kumbukirani Iye anati, “Muzipenyerera ndi kupemphera.”

Tizichita gawo lathu. Musamufuse Mulungu kuti achite gawo lake kupatula ngati inu mutachita gawo lanu. Chisomo chake ndi chokwanira. Iye amapereka nyonga mu zinthu zonse. Paulo anati, “Ine ndikhoza kuchita zinthu zonse kudzera mwa Khristu zondilimbikitsa ine.”

Nthawi zonse muziganiza monga Khristu amaganizira. Baibulo limatiuza ife kuti tizilora kuganiza uku kuzikhala mwa ife monga kunali mwa Khristu. Njira yokhayo yokhalira moyo wochita bwino kwa Mulungu ndi kudzikana wekha kwa dziko ndi zonse ziri mmenemo. “Ngati munthu aliyense anganditsate Ine,” Yesu anatero, “iyeyo ayambe wazikana yekha, natenga mtanda wake nanditsata Ine.” Akhristu ambiri amalephera posakula mu chisomo ndi chidziwitso cha Khristu tsiku ndi tsiku, posawumbidwa monga mwa moyo Wake, ndi pophunzira njira Zake. Iwo amayamba bwino, koma samatha kuchipanga icho chinthu cha tsiku ndi tsiku. Ngati sitingachipange icho chinthu cha tsiku ndi tsiku, ndiye kuti talephera.

Njira imodzi yophweka yovulazidwira ndi mphamvu za Satana ndi podzimana tokha madalitso ndi mwayi zomwe zaperekedwa kwa ife mwa Khristu Yesu, Ambuye wathu. Ichi, zoona, chikutanthauza zinthu zonse za ku moyo zomwe ife talandira kwa Iye, zomwe ziri mwayi woitanira pa Mulungu pa vuto lirilonse la moyo. Kulephera kukhulupilira mu chisomo ndi chifundo Chake, ndi kulephera kuti tiwadziwe Mawu Ake kapena malonjezo otiyenera ife, zikutanthauza kuti tipyerera mdzanja la Satana chifuwa chosowa chikhulupiliro, chidaliro, ndi chidziwitso, koma ngati ife tiwadalira Ambuye ndi mtima wathu wonse, ndiye adzakwaniritsa malonjezo Awo. Musangalale mwa Ambuye, ndipo Iye adzakupatsani inu zokhumba za mtima wanu, pakuti zinthu zonse ndi zanu chifukwa cha Khristu, ndipo sadzamana chabwino chirichonse kwa iwo amene akuyenda molungama.

Iwo amene akhazikitsa malingaliro awo pa Khristu Yesu adzakhala nawo mtendere wangwiro, kotero mukhuthule zanu zonse kwa Mulungu. Muzimukonda Iye ndi mtima wanu, mphamvu zanu, moyo wanu, malingaliro anu ndi thupi lanu, ndipo muzikumbukira njira yopachikidwa ndi njira yokhayo. Paulo anati, “Ine ndapachikidwa kwa dziko, ndipo dziko lapachikidwa kwa ine ndi thupi la Yesu.” Musakonde dziko lapansi, ngakhale zinthu ziri mu dziko. Mutsatire chilungamo! Funani funani ufumu wa Mulungu, ndipo zinthu zina zonse zidzawonjezekera kwa inu, zomwe inu mukuzisowa mu moyo uno.

Zolembedwa ndi George Leon Pike Sr.

Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.

Chiyero Kwa Ambuye

Uthenga uwu umasindikizidwa kuti uzigawidwa mwaulere. Ngati mukufuna matraki ambiri chonde mulembere mu Chizungu ku adiressi ili pansipa.

CHM9914T • CHICHEWA (MALAWI) • THE CRUCIFIED WAY