Mkuntho wa Moyo


Mu dziko lino, ife, ngati anthu, nthawizonse timakhala tikuthamangira mu mikuntho ya moyo pa nyanja ya mafunde a mantha, masautso, chiwonongeko ndi zosokoneza.

Ngati inu mutayang’anitsitsa pa zinthu izi, inu mudzawona chinthu chimene Yesu ankachinena polankhula za munthu yemwe anamanga nyumba yake pa thanthwe. Ukatha mkuntho uliwonse, pamakhala zinthu zowonongeka, koma nthawizonse kwa munthu yemwe moona wakhalira moyo Mulungu ndipo ali nacho chidziwitso choona cha Mulungu, iye nthawizonse amakhala mgonjetsi.

Iye akhoza kukankhidwa ndi mphepo zotsutsa za chiphunzitso, mantha, ndi zokhumudwitsa, komabe iye samasochera. Paulo analankhula za anthu ena amene asochera mu chikhulupiriro. Chifukwa chake ndi chakuti iwo sanamange chikhulupiriro chawo pa Mawu a Mulungu, Thanthwe, Yesu Khristu.

Paulo ankanena za Thanthwe mu masiku a Mose, kumene ana a Israeli ankalandira madzi kuti athetse ludzu lawo. Iye anati Thanthwe limene linkawatsata iwo linali Khristu.

Mzanga, mikuntho ya moyo ndithudi ibwera, ndipo mizimu yozunza izibweranso, pa nthawi ina kapena imzake idzakukanthani inu. Chotero, kukanakhala bwino mukanakonzeka ndipo mukonze chombo chanu pofuna kukhala wotsimikiza kuti palibe pobowoka.

Woyendetsa ndege wabwino amaiyang’ana ndege yake bwinobwino asanayambe kuwuluka. Amafufuza mafuta ndi kukhala wotsimikiza kuti ali nawo mafuta wokwanira. Kuyang’ana koyendetsera ndi kutsimikiza kuti zinthu zonse zikugwira bwino ntchito.

Baibulo limatiuza ife kuti munthu wochenjera amasamalitsa kumene iye akupita. Muchitiretu izi pamene dzuwa likuwala, pakuti pakuwuluka mu ndege kapena pakuyenda panyanja, inu simudzakhala nawo mwayi. Yesu anati muwerengero mtengo wake ndi kukhala woyembekezera ndi kupemphera!

Zolembedwa ndi George Leon Pike Sr.

Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.

Chiyero Kwa Ambuye

Uthenga uwu umasindikizidwa kuti uzigawidwa mwaulere. Ngati mukufuna matraki ambiri chonde mulembere mu Chizungu ku adiressi ili pansipa.

CHM9910T • CHICHEWA (MALAWI) • LIFE’S STORM