Mawu A Mulungu Ochiritsa


Kwa onse amene sanamvepo kukoma kwa moyo wochuluka wa Mulungu.

Chinthu choyenera kudziwa ndi chakuti Mulungu ndi Mzimu wa moyo. Mwa Iye, mulibemo imfa. Satana ndiye Mzimu wa imfa, ndipo mwa iye mulibemo moyo. Mulungu anapereka moyo wosakhalitsa, ndipo tonsefe tiri otenga nawo omwe tabadwira mu dziko lino. Ife timapuma ndi kumamva kukoma kupuma kwabwino kwa moyo. Moyo ungakhale wokongola bwanji kwa iwo omwe alibe maganizo okayikira ndi a chikhulupiriro! Ndi zabwino bwanji, kumangoyenda mmisewu, kapena kuyenda maulendo kuzungulira dziko" kuona nthaka yokongola ndi maluwa, zonse zamoyo ndiponso zamoyo woona ndi kukoma kwache, ndiponso mafunidwe opatsidwa kwa izo ndi dzanja la Mulungu" ndi kukhala ndi thanzi likuyenderera mu mthupi lanu, popanda malingaliro otsutsana a kudandaula, kumverera kwa matenda akuyenderera mthupi lanu" maganizo anu, akuyenda mu mzimu wanu, zikubweretsa chikondwerero chachikulu.

Indetu, zikunenedwa bwino ndi wolemba, kuti timatunga madzi kuchokera mzitsime za chipulumutso ndi chikondwerero" kuti tikalowe zipata Zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo Ake ndi chilekemekezo. Bukhu limatiuza ife kuti, iye amene ali ndi mtima wokondwera amakhala nacho chikondwerero chosatha, ndipo mtima wokondwa umachiritsa ngati mankhwala, koma mzimu wosweka umaumitsa mafupa. Tikuuzidwa ndi wolembayu kuti chisoni chimachita imfa. Aliyense angathe kuona poyera chimene Baibulo likuphunzitsa kuti kumtumikira Mulungu ndi chimwemwe, mtendere ndi chilungamo mwa Mzimu Woyera. Ichi ndi chifukwa chake chikhulupiriro mu malonjezo Ake olembedwa, mu Mawu Ake osakayika, osalephera, amene akuchokera ku nthawi yosatha kufikira ku nthawi yosatha, amene sasintha, amabweretsa moyo wosatha.

Ndiwo Mawu odzoza ndi moyo, malonjezo a ziyembekezo ndi achikhululukiro, kumulola yense yemwe angafune, abwere. Ndiwo malonjezo amachiritso kwa onse. Monga mwa chikhulupiriro chanu, chomwecho zikhale kwa inu mosalemekeza munthu, koma kuwasamalira anthu onse monga zolengedwa za Mulungu. Timadzisankhira tokha komwe tikupita.

Kodi munthu angakhale bwanji ndi moyo wamphumphu? Pali njira imodzi yokha. Mulungu sanatipatse ife Mzimu wamantha. Sitinabadwe ndi mantha, koma mzimu wa ziwanda umene umabwera mu mzimu wathu kudzera mu njira ya kusakhulupirira pa Mawu a Mulungu ndi malonjezo Ake amene anatilenga ife ndipo amatisunga ife kufikira moyo.

Yesu anati, “Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.” Ziri kwa ife kugwiritsa ntchito mbali ina ya moyo kuti tipange chikhulupiriro chabwino mu mawu olenga a Mulungu. Monga momwe maganizo athu ali nacho chikhulupiriro chodzala ndi zoganiza zathu, chomwechonso maganizo a Khristu ali nacho chikhulupiriro chimene chinapatsidwa kwa oyera mtima, monga mmene Mulungu anawapatsa maganizo a Khristu. Tiyenera tikangamire chikhulupiriro cha Yesu Khristu. Paulo anati, “Tiri nawo mtima wa Khristu.” Koma tiyenera kuupatsa mtendere. Mu mtima umenewu okhala mu Mzimu wathu kapena mu mtima, Mulungu amamasula zonse zimene ali nazo mu mphamvu Zake, kudzera mu mzimu wake kubwera mu thupi lathu" monga momwe chidzera chipulumutso, machiritso, ndi zina zotere. Ufumu wa Mulungu uli mkati mwathu, kotero machiritso athu ali mkati mwathu, monganso chipulumutso chathu.

Paulo anati, “Ndife thupi la Khristu.” Ambiri agona, chifukwa alephera kuzindikira izi. Yesu anadzakhala wodwala pa inu, thupi linatunduzidwa mu imfa pa mtanda, kuti inu mukakhale thupi Lake ndiko kukhala mfulu kwathunthu kwa tchimo ndi matenda. Mumachita izi mwa chikhulupiriro mu imfa ya Khristu, pozindikira kuti Iye anafa mmalo mwanu kuti mukakhale thupi Lake mu moyo. Ngati mchikhulupiriro, mwakhulupirira kuti Iye anatenga malo anu, nthawiyomweyo mumachiritsidwa. Nthawizonse muzikumbukira kuti thupi lanu, limene linali pansi pa themberero la chilamulo cha chiweruzo cha Mulungu kwa Mose, linapachikidwa pa mtanda, ndipo pakuti ndinu tsopano thupi la Khristu, ndinu omasulidwa ku themberero ndi chikhulupiriro chanu mwa Yesu.

Pangano la Mulungu ndi malonjezano Ake onse ndi a Ambuye Yesu. Timazilandira izo mchikhulupiriro mwa Yesu. Pokhulupirira kuti ndife thupi la Khristu, zimapangitsa malonjezo kukhala athu. Kumbukirani kuti chikhulupiriro chathu ndi kuganiza kwaluntha komwe kumayanjana ndi Mawu a Mulungu. Mawu a Mulungu ndiwo mtima wa Khristu. Chikhulupiriro chimadza pakumva Mawu. Chikhulupiriro cha Khristu ndi chitsimikizo chachikulu mu mtima mwathu kapena mzimu. Kukhulupirira kuti ndife opulumutsidwa kapena tinachiritsidwa mwaluntha zimangotanthauza kuti tinamizidwa ndife onyengedwa ndipo tinataika. Zimayenera kukhala kukhudzidwa kwa mtima kapena mzimu. Ndi mtima munthu amakhulupirira kufikira ku chilungamo, mdiponso monga munthu asinkha mkati mwake ali chomwecho. Yesu anati, “Ngati mwakhulupirira mu mtima mwanu ndipo osakaikira" mudzakhala nazo zonse zimene mupempha.” Mtima sudzakhulupirira popanda kutsimikizidwa ndi kudzipereka kwanu, ndi mphamvu zanu ku Mawu a Mulungu. Ndi chifukwa chake chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa. Ntchito zimawutsa chidaliro chanu mu chisomo cha Mulungu kwa inu.

Chikhulupiriro cha Khristu mwa inu chachoka ku zipsyinjo zauzimu, pamene mphamvu zisanu za thupi lanu (kupenya, kulawa, kumva, kununkhiza, ndi kukhuza) zafa, kudzera mu kusala kapena kudzipereka. Satana alibe njira yogwirira ntchito ngati wachotsedwa mwa inu, kupatula akadzera mu mphamvu zisanu kuti akatchinge chikhulupiriro chanu. Tsopano popeza tikumva izi, tiyeni timange chikhulupiriro chathu pakumva Mawu amalonjezo Ake kwa ife.

Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chirichonse monga mwa chuma Chake mu ulemerero. Kumbukirani, kuti ngakhale zathupi, ndalama, kapena zauzimu, Iye adzakupatsani zonsezo. Ine ndine Mulungu amene ndikhululukira mphulupulu zako zonse, ndipo ndimachiritsa nthenda zako zonse. Mukudziwa, Iye anati zonse! Ndidzachotsa matenda pakati pa iwe, kapena kuchotsa mu mzimu wanu.

Mulungu ndi moyo, ndi zonse za mmoyo, monga ngati machiritso, chipulumutso, chikondwerero, mtendere, ndi kulemera, zimene ziri za Mzimu wa moyo ndi thupi la Khristu, zomwe thupi lake ndi inuyo. Yesu anati, “ndinadza kuti mukhale nawo moyo.” Kuganiza chotere, ndi mtima ndi chikhulupiriro cha Khristu, kudzera mmenemo ukoma umayenda momasuka, Kodi sadzatipatsa, Khristu, kwaulere zinthu zonse? Paulo anafunsa.

Mzimu wa Satana ndi imfa: mdani wa Mulungu. Malemba amatiuza ife, kuti imfa inabwera ndi munthu. Zooneka za imfa ndi mantha, ukali, chisoni, kudandaula, usiwa ndi matenda. Zonsezi ndi adani a Mulungu. Khristu anabwera kudzatsutsana nazo zinthu zonsezi: Mliri, nthenda yowondetsa ya chifuwa, malungo, chibayo, kutentha thupi, zirombo, chisinkwi, chinoni, nthenda yotaya magazi, chipere, mphere, khungu, chironda choipa chosachira nacho kumaondo ndi miyendo, ndi nthenda yonse, yosalembedwa mbukhu la chilamulo ichi, unamasulidwa kwa iyo. Zonse zinali mu themberero la chilamulo. Muli achisomo. Khristu anakhala themberero chifukwa cha ife. Anatiombola ife ku themberero ndi thupi lake pa mtengo.

Kudwala konseku ndi matenda, zodziwika mdziko lonse, zinabwera chifukwa cha tchimo. Tchimo lija linali kusakhulupirira Mawu a Mulungu. Eva anachimwa tchimo ili. Chinthu chosatuluka mu chikhulupiriro, ndicho tchimo. Adamu anabweretsa anthu onse ku themberero pa mulandu wopanda chikhulupiriro. Khristu anaombola anthu onse ku themberero mu chikhulupiriro. Mwa Adamu, onse akufa, mwa Khristu, onse ali nawo moyo.

Anatuma mawu Ake (Yesu) ndipo anawachiritsa iwo. Chikhulupiriro mu Mawu Ake, zimachititsa Mawu kukhala thupi. Timakhala mawu, kalata, yodziwika ndi yowerengedwa ndi anthu onse, Mawu a Mulungu anapangidwa thupi. Timakhala mmodzi ndi Mawu monga thupi la Khristu. Mulibemo matenda mwa Mulungu. Ndi mikwingwirima Yake, munachiritsidwa.

Mumakhala nacho chikhalidwe cha Khristu. Anamulaka Satana ndi mawu a umboni wawo ndi mwazi wa Mwanawankhosa, ntchito ya pa Gologota, akuvomereza, mu mawu ndi mu ntchito, zomwe Iye anawachitira iwo. Musamadalile kumvetsa kwanu, muzidalira mwa Ambuye (Mawu) ndi mtima wanu wonse.

Tizibweretsa ganizo lirilonse kuti lizilamuliridwa ndi Khristu, tizitaya zolingalira, mantha, ndi kukayikira, tikatero tikuwononga maganizo aumunthu omwe ali mdani wa Mulungu. Mulungu sangasinthe chinthu chimene chaturuka pakamwa Pake. Iye amapenyerera kuti awawone Mawu Ake akuchitika.

Ngati, ndi mikwingirima Yake inu munachiritsidwa, ndipo Iye samalemekeza anthu, aponso ife tiyenera kumazitchula zinthu zimene palibepo ngati kuti ziripo (tisamadalire kupenya kwa maso: olungama adzakhala moyo ndi chikhulupiriro), kotero chikhulupiriro chako chakuchiritsa iwe.

Mulungu amatiuza mMawu Ake, “Ndipemphera kuti pa zinthu zonse mukhale olemera komanso athanzi, chimodzimodzi monganso miyoyo yanu ikuchita bwino.” Kulemera kwa thanzi lanu kumalamuliridwa ndi kulemera kwa moyo wanu. Ndi Ambuye, Mulungu wanu, amene amakupatsani inu mphamvu yoti mulemere. Muzipereka chuma chanu chimene muli nacho ku ntchito ya Mulungu kuti mukasinthanitse ndi chuma chamuyaya.

Muzikhulupirira (muzikumbukira, kutsutsidwa kwa mtima) kuti matenda anu achokadi zoona. Sizingalephere ngakhale nthawi imodzi. Inu mukhoza kuzipangitsa kuti mukukhulupirira ndipo nkukhalabe chidwalireni, koma, ngati inu mukukhulupirira zenizeni, izo zidzalamulira thupi lanu, ndi kulikakamizira ilo ku ntchito za chilungamo ndi ntchito zokhala nawo umboni. Mulungu samatisiya ngakhale kutitaya ife. Mulungu samalephera. Ife timamusiya iye chifukwa cha kusakhulupirira. “Muzipempha ndi chikhulupiriro, osakayika,” Yesu anatero. Yohane anati, “Ichi ndi chitsimikizo chathu mwa Iye: chimene tipempha mu dzina Lake, timalandira. Ngati mtima wathu sutitsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu.” Paulo anati, “Mmenemonso ndiziyenera ndekha ndikhale nacho nthawizonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.” “Yense wakupempha alandira,” atero Malemba. Yesu anati, “Chirichonse mupempha mu dzina Langa, ndidzakuchitirani.” Yesu anati pofuna kulemekeza Atate mmwamba. Muzipempha, kuti chimwemwe chanu chikakwaniritsidwe. Iye ananyamula nthenda zanu ndi zisoni mu thupi Lake pa mtengo, ndipo ndi mikwingwirima Yake, inu munachiritsidwa. Yesu anati, “Kwatha.” Ngati Iye ananyamula izo mthupi Lake chifukwa cha inu, ndiye mukuzinyamuliranjnso izo chifukwa cha bodza la Satana?

Kumbukirani, chikhulupiriro ndi kugonjera kwa maganizo anu ndi kumufuna kwanu Iyeyo. Kukhulupirira Mawu Ake, ndi kuwakana maganizo anu ndi kumverera komakwiya. Kumaganiza maganizo ovomereza a malonjezo Ake kungachotse mmalingaliro anu maganizo otsutsa ogonja, ndi kubweretsamo chikondwerero, thanzi ndi kulemera kwa inu. Ngati musiya kukhulupirira izo zimaleka kugwira ntchito. Nthawizonse muzipenyerera maganizo anu. Mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu. Muziganiza maganizo anu enieni maganizo a Khristu, ndi kutsimikizira icho chimene chiri chabwino ndiponso chovomerezeka kwa Ambuye. Iyeyo ndi wansembe wamkulu, wokhudzidwa ndi zomverera za zifooko zathu, amatikhalira pakati ife"wansembewamkulu wachivomerezo chanu.

Ndi mtima, munthu amakhulupirira ku chilungamo. Chivomerezo chimapangidwira ku chipulumutso ndi pakamwa. Vomerezani, mukhulupirire ndipo muchiritsidwe mu dzina la Yesu Khristu, muchoke ku zofooko zanu zonse, ndi matenda, ndi zigonjetso. Mulungu akudalitseni inu ndiro pemphero langa.

Zolembedwa ndi George Leon Pike Sr.

Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.

Chiyero Kwa Ambuye

Uthenga uwu umasindikizidwa kuti uzigawidwa mwaulere. Ngati mukufuna matraki ambiri chonde mulembere mu Chizungu ku adiressi ili pansipa.

CHM9908T • CHICHEWA (MALAWI) • GOD’S HEALING WORD