Musachiwope Choipa


Ndikufuna kuti ndiyambe phunziro lathu ndi kukambirana pokufunsani funso ili: kodi ndinu wokondwa kwenikweni, kapena kodi inu muli mu ukapolo wauzimu zimene mukudandaula nazo ndi kumaziwopa? Mukudziwa, alipo anthu ambiri amene amadzipangitsa kuti akukondwa, koma ndapeza kuti, ineyo ngati mtumiki, kuti anthu ambiri sikuti ndi osangalala ayi. Chimandinjenjemeretsa kuti ndifotokoze moyo weniweni. Timauzidwa ndi mmodzi wa olemba a mu Baibulo, kuti pamene Khristu, yemwe ali moyo wathu, adzawonekere, ndiye ndi pamene ife tidzayambedi kukhala moyo.

Pamene anthu abadwa mu dziko lino, iwo amabadwira ku imfa. Anabwera mu dziko lino kwa cholinga chimodzi, ndipo icho ndichakuti adzafe. Paulo ananena, mu Malemba, kuti moyo wathu wonse ife timagonjera ku ukapolo chifukwa cha kuiwopa imfa" koma kodi inu mukudziwa, kuti pamene munthu abadwira mu ufumu wa Mulungu, iye amabadwira ku moyo, kuti akakhoze kubadwa mu malo a zenizeni? Iye samawopanso imfa chifukwa chakuti wadutsa kuchokera ku imfa wapita ku moyo. Ambuye amafuna kuti anthu azikhala moyo wamphumphu wosatchingidwa ndi mantha. Amatiuza ife mu Mawu Ake kuti mitima yathu isamavutike.

Ichi, ndithudi, chimatidziwitsa ife kuti tiri nayo mphamvu kuti mitima yathu isamavutike. Palibe chifukwa kuti tiziitanira pa Mulungu ndi kumupempha Iye kuti atichitire ife chinachake chimene ife tikhoza kuchita, koma kuti tizimupempha mphamvu kuti tizikhoza kuchita chimene Mulungu watipatsa ife kukhoza koti tichite. Njira yotetezera mitima yathu ku mantha ndi zopsyinja za moyo ndi kukhala ndi malonjezo a Mulungu a chikondi ndi kukhudzidwa nafe, ndi kuika chidaliro chathu chonse mwa Iye, kudalira mwa Iye ndi mtima wathu wonse, ndipo Iye adzakwaniritsa izo.

Davide anati, “Ine sindidzawopa choipa chirichonse.” Yesu akutiuza ife mu Mawu Ake, “Mtima wanu usavutike.” Mulungu sanatipatse ife mzimu wa mantha. Mantha ndi a mdierekezi. Ife tisamawope umphawi, chifukwa umphawi ndi woipa, ndipo kuwuwopa iwo ndi kusowa kwa chikhulupiriro mu Mawu a Mulungu, pakuti Iye ananena kuti Iye adzayesetsa, pamwamba pa zinthu zonse, kuti ife tidzalemere ndi kukhala ndi thanzi, chimodzimodzi pamene miyoyo yathu ikutukuka.

Kusakhulupirira ndi kusamukhulupirira Mulungu. Icho chimene sichiri cha chikhulupiriro ndi tchimo, pakuti ife timayeretsedwa ndi chikhulupiriro, kapena timapulumutsidwa mwa chisomo kudzera mu chikhulupiriro. Kuwopa matenda ndi kusakhulupirira mu Mawu a Mulungu, pakuti Malemba amatiuza ife, “Ine ndine Mulungu wanu, yemwe amakhululukira mphulupulu zanu zonse, ndi kuchiza nthenda zanu zonse.” Kumbukirani, ife sitimayenera kuti tiziwopa kubwerera mmbuyo, ndipo palibe chimene chingatilekanitse ife ku chikondi cha Mulungu. Ngakhale Satana alibe mphamvu yoti achitire izo. Ngati inu mukuchita izi chifukwa Satana akukuyesani inu kuti muzisilira tchimo, izo zikutsimikizira, molingana ndi Baibulo, kuti inu simunayambe mwamuwonapo Mulungu kapena simukumudziwa Iye. Kotero, ife tikukhoza kuwona chitetezero chamuyaya mwa Iye. Inu mudzataya chikondi cha dziko lino ndi zonse zomwe ziri mmenemo pamene munthu wakaleyo wafa, ndipo munthu watsopano yemwe wavala Khristu adzakonda zinthu zakumwamba. Zokambirana zake zidzakhala zoyera, pakuti iye ndi cholengedwa chatsopano. Taonani, zinthu zakale zatha, ndipo zinthu zonse zasandulika zatsopano, likutero Baibulo.

Davide wakale anati, “Ine ndinawafuna Ambuye ndipo Iye anandimva ine, ndipo Iye anandipulumutsa ine kwa mantha.” Mukuloleranji malingaliro a Satana kubwera mu mtima mwanu, kuti azifooketsa chikhulupiriro chanu ndi mantha, kudandaula, ndi kukaikira? Kodi azichita kukukankhani inu mopitirira maganizo anu, Mulungu anatero, “Ine sindidzakulolani inu kuti mudzayesedwe kuposa muyezo wanu, koma ndi mayeserowo ndidzapanga njira yopulumukirapo, kuti inu mukakhoze kudutsamo izo.” Iye akutiuza ife kuti tiponyere pansi malingaliro aliwonse, ndi kuwabweretsa malingaliro aliwonse kuti agonjere chikhulupiriro, ndi kudalira mu Mawu Ake.

Muzikana zomverera zanu, ndiponso muziwakana malingaliro anu. Muziyankhula ndi kuganiza Mawu a Mulungu! Muziwakhala moyo iwo! Muziwakonda iwo! Muziwalankhula iwo! Muziwaimba iwo! Chikhale chokhumba cha mtima wanu, ndipo pamene mukhazikitsa mtima wanu pa Yesu Khristu, inu mudzakhala nawo mtendere wangwiro. Kulibeko mtendere kwa woipa. Iye ananena kuti ife timayeretsedwa mwa chikhulupiriro mu Mawu Ake, kotero, monga Yesu anati, “Musawope ayi!”

Kuti inu muziwopa mphamvu zinazo ndiye kuti inu mukuzimvera mphamvu zimenezo, ndipo potero, izo zimakhala bwana wanu, ndipo inu mumakhala kapolo pakuti izo zikukuikani inu mu msinga

Zolembedwa ndi George Leon Pike Sr.

Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.

Chiyero Kwa Ambuye

Uthenga uwu umasindikizidwa kuti uzigawidwa mwaulere. Ngati mukufuna matraki ambiri chonde mulembere mu Chizungu ku adiressi ili pansipa.

CHM9907T • CHICHEWA (MALAWI) • FEAR NO EVIL