Zinthu Zomwe Zili Zosalira


Mu maulendo anga ndaona zithu zambili ndipo ndi nakambilana ndi akulu akulu ndi oziwa malamulo apingo ofunika. Ndaona bvuto lalikulu kwa anthu amulungu pa moyo wao, buhku lopatulika litiuza kuti anthu ali oipa ndi owonongeka chifukwa cakusaziwa Hoseya 4:6 ichi ndi chimene ndachiona.

Anthu sakuziwa colinga cha mulungu ngakhale cofuna chace, chifukwa caichi satana wapeza malo mwaiwo. Bukhu lopatulika likuti tisapase satana malo koma timusase ndipo azathawa kwaife. Yesu anati ziwani kuti ndikupasani mphavu zoposa za mdaniyo ndipo chifukwa chaici palibe chingakuonongeni.

Davite anati mtima wanga sungasithe pa mulungu ndipo khani zoipa sizingandivutise ine. Muloto ndinaona satana. Poyamba satana anandizela, koma ndinali ndi chikhulupilo ndipo ndinamususa ndipo anatuluka ngati thumba lapweya long’ambika ng’ambika. Yesu anati, musaope! Mulungu sanatipasa mzimu wa mantha ai, nanga chifukwa chiyani tingaulole wocokela kwa satana? Anthu amaopa matenda, umphawi ndi kuvutika. Anthu amaopaso kutaika kwa zinthu zapasi pano.

Mvesani ndikugawilani bukhu lopatulika, opani mulungu amene mizimu yose ipita kwaiye m’dziko. Malingalilo akilistu ndi kumasata satana pamoyo uno I Akolito 13:11-13 zopindulisa inu, coyamba kumbukilani, ndipo maganizo anu kuti mulungu samasamala za munthu monga mwa malemba kuti comwe mulungu acita kwa ena azacitaso kwa iwe kumbukilani mulungu a mapasa ndipo anati, palibe cosatheka kwa mulungu.

Choncho zindikilani kuti, zonse zimapelekedwa kwaiwo okhulupilila. Conco sicifukwa cakupeza kwanu. Izi sizithandiza kuti zinthu zose ndizotheka kubwelesa ufumu wa mulungu mwabwino koma mwa mkilistu. Chikilistu ndi cikhulupilo kuti anapacikidwa, tingathe kucita cilicose.

Bukhu lopatulika likuti, mulungu mosasamala zamunthu amakhululukira machitidwe athu oipa, ndikuchiritsa matenda anthu. Bukhu lopatulika limatiuza kuti mulungu ndi wabwino ndipo palibe wabwino koma mulungu, conco mulungu sanyozeka.

Bukhu lopatulika likuti Yesu Kristu amene anabadwa mwathupi la munthu, anabadwa kuzacita zithu zabwino ndi kuciza onse anali olamulidwa ndi mzimu wasatana woipa. Mumaziwa kuti ngati bukhu likuti “onse,” iye sakasamala za akupemphela kapena akunja. Iye akafuna cikhulupililo.

Sopano iye anati mufuna ucimo umene unalipo kale wa ana asatana? Ngati mufuna kulandira mphaso yopanda chilungamo ndi chiyeleso, comwe chiri ngati covala caukwati muzapezeka malingalilo acikondi ndi chifundo, kumene kuli kuwala kwa dziko, malingalilo akilistu ndikumasata za satana kamba chamantha ndi masauso, zomwe zili kunja kuno. Mudima pamozi ndi kulingalila zacilengedwe ca mulungu ndi kukhulupila za anthu ndikukhala opanda mphavu wokhulupila boza ndicitaiko.

Ndipo anati, yenda njila ndipo usacimwe, opa zoipa ndi kuzicita zomwe zikhuza iwe. Koma ngati utabadwa kawili ndikukhala wotembenuka mtima kumacimo ndi njila zako ndikuzazidwa ndi zimu wace, koma uzacoka kupita kumoyo wosatha, koma ucokela kuifa, kumeneko matenda kulibe ngakhale imfa. Sikulilidwa ndi covuta cilicose, kulibe, koma cikhulupililo cikhale bwino kuti tisayesedwe ndi satana ndipo kuti angathe kufala thupi mwathu ngati sitisintha. Cimo lingadulidwe cifukwa cazolakwa zathu ndi kulephela kwathu cifukwa umunthu wathu wakale unapachikidwa pa mozi ndi kilistu Yesu patanda. Cifukwa cace tisafune zadziko monga kuba, kulezela, misece, mitala, kufuna zaini, mowa, kacaso, kusinjilila, kupha, simukalowa kumwamba. Kapena ukilistu wanu ndi wongovala ngati malaya, kapena kufuna kuimbilidwa nyimbo mukafa. Ai simukalowa ku mwamba. Yesu afuna inu mukakhale naye komweko.

Asakunyengeni munthu kapena chalici kuti chakudya sichiipitsa. Anthu akuipa monga Jenesesi 3-1. Paka 7 ndiposo I Akolito 6:8. Pakavesi 10 kulezela kacaso numeri 6-1-paka 3. Abale azanga amene mumati mwalandila Yesu, abusa, akulu amipingo, akilistu, samalani boza monga havo anavela boza, tose talowa m’mavuto, matenda, ifa, usiwa, njala umphawi, zosezi talandila chifukwa caboza. Yesu ati khulupilani ine, ndipo musiye zose mukalandi lemoyo wosatha kumwamba. Zangawe ulipati, kumoyo wosatha kapena kucilango cosatha? Cenjelani.

Ndine Rev. George Leon Pike Sr.

Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.

Woyera Kwa Mulungu

Uthengawu wadindidwa kuti ugawidwe kwa ulele. Ngati mufuna kulandira zambiri, mutha kulembera ku adilesi ili musiyi, ndipo mutiuze matraki angati mungawagwiritse ntchito mwa nzeru.

CHE9917T • CHICHEWA/NYANJA • THINGS THAT REMAIN