Mau Amulungu Amaciritso


Kwa onse amene sanamve macurukidwe a umoyo mwa Mulungu.

Cinthu choyenera kudziwa, ndicakuti Mulungu ndiye Mzimu wa moyo. Mwa iye mulibe imfa. Satana ndiye Mzimu wa imfa, ndiponso onse obadwa mdziko lino ali nao. Tipuma ndikumva mpweya wabwino wa moyo. Oo! kodi ubwino wamoyo ungakhale wa mtundu otani kwa iwo amene sali ndi mabvuto amaganizo okayika ndi a cikhulupiriro. Ndiubwino otani umenewu, kuyenda cabe mumiseu, kapena kuyenda maulendo kuzungulira dziko" kuona nthaka yokoma ndi maluwa, zonse zamoyo, ndiponso ndizamoyo woona ndi kukoma kwace, ndiponso mafunidwe opatsidwa kwaiwe ndi zanja la Mulungu" ndi kukhala ndi thanzi, kucokera mthupi lako, ndikukhala opanda mabvuto ndizoganiza zokayika mwaife, ndikukhala opanda maganizo ankhawa" kusamva kudwala mthupi lako" maganizo ako, oyenda Mumzimu wako, abweretsa cikondwerero cacikuru.

Indetu, zinenedwa zokondweretsa kuolemba, kuti titunga madzi m’zitsime za cipulumutso, ndi cikondwerero (Yesaya 12:3). Kulowa ku zipata zace ndiciyamiko, ndi kumabwalo ace ndi cilemekezo (Masalmo 100:4). Bukhu Lopatulika litiuza ife, “mtima wosekerera uciritsa bwino" koma Mzimu wosweka uphwetsa mafupa.” Tauzidwa ndi malimba kuti cisoni cicita imfa. Aliyense angathe kuona poyera cimene bukhu lopatulika liphunzitsira kuti kusewenzera Mulungu ndi cimwemwe, mtendere ndi cilungamo mwa Mzimu woyera. Ici ndi cifukwa cace cikhulupiriro mumalemba amalonjezo" ndi kusakayika mu Liu losalephera, limene licokera kunthawi yosatha kufikira kunthawi yosatha, limene silisintha, kubweretsa moyo wosatha.

Ndiwo mau a Mzimu ndi moyo, malonjezo a zoyembekeza ndi acikhululukiro kuti, “onse amene angafune, abwere.” Ndi malonjezo amaciritso kwa onse. Monga mwa cikhulupiriro cako, cicitidwe kwa iwe, kulibe tsankhu, koma kwa munthu aliyense ciziwike kuti anapangidwa ndi Mulungu. Tizisankhira ife tokha kopita.

Kodi munthu angakhale bwanji ndi umoyo wa bwino? Kuli njira imodzi cabe. Mulungu sanatipatse Mzimu wamantha. Sitinabadwa ndi mantha, koma ndi ziwanda zimene zibweretsa mu Mzimu kamba kosakhulupira mau a Mulungu ndi malonjezo amene anatipanga ife ndi kutisunga kumoyo.

Yesu anati, “Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha.” Cilikwa ife ku dzera mbali ina ya moyo, kapena ku panga njira ya bwino ya cikhulupiriro mu mau a Mulungu amalengedwe. Monga m’mene maganiz o athu ali naco cikhulupiriro cotsatana ndi zoganiza zanthu, moteronso maganizo a Kristu ali naco cikhulupiriro cimene cinapatsidwa kwa oyera mtima, monga m’mene Mulungu anawapatsa maganizo a Kristu. Tiyenera kukhala acikhulupiriro ca Yesu Kristu. Paulo anati, “Tiri nao Mtima wa Kristu.” Koma tiyenera kuupatsa mtendere. Mumtima umenewu okhala mu Mzimu wathu kapena mumtima, Mulungu amasula zonse zimene zili M’mphamvu yace, kudzera mumzimu wace kudza m’thupi lathu" monga momwe cidzera cipulumutso, maciritso, ndizina zotere.

Ufumu wa Mulungu uli mkati mwaife ndiko kuti, maciritso athu ali mkati mwa ife, monganso cipulumutso cathu.

Paulo anati, “ndife thupi la Kristu.” Ambiri agona, cifukwa alephela kugawa paici. Yesu anadwala pa iwe, thupi linatunduzidwa, mu imfa yapamtanda, kuti ukhale thupi lace, ndiko kuti ukhale opanda cimo ndi matenda. Mu cita izi zonse ndi cikhulupiririo mu imfa ya Kristu, kugawira kuti anafa m’malo mwanu, kuti ukhale thupi lace mu moyo. Ngati m’cikhulupiriro, wakhulupirira kuti anatenga malo ako, nthawi imeneyo udzaciritsidwa. Masiku onse ukumbukile kuti thupi lako limene linali ndi temberero cilamulo ca ciweruzo ca Mulungu kwa Mose, lina pacikidwa pa Mtanda, tsono popeza ndiwe thupi la Kristu, unamasulidwa ku temberero ndi cikhulupiriro cako mwa Yesu.

Cipangano ca Mulungu ndi malonjezano ali kwa Ambuye Yesu. Tizilandila izi m’cikhulupiriro mwa Yesu, Pa kukhulupirira kuti ndife thupi la Kristu, tipanga malonjezo kukhala athu. Kumbukila kuti cikhulupiriro cathu ndi camu Mtima ndi maganizo otsatana ndi Mau a Mulungu. Mau a Mulungu ndiwo Mtima wa Kristu. Cikhulupiriro cidza ndi kumva mau. Cikhulupiriro ca Kristu ndi citsimikizo cacikuru mumitima yathu kapena Mzimu. Kukhulupirira kuti tapulumuka kapena kuciritsidwa munzeru zathu kutanthauza kuti tanamizidwa ndi kusoceretsedwa. Chiyenera kukhala citsimikizo ca mu Mtima kapena mu Mzimu. Ndi Mtima Munthu akhulupirira kutengapo cilungamo. Ndiponso, ati monga munthu asinkha M’kati mwace ali votere. Yesu anati, “Ngati wa khulupirira mu Mtima wako ndiponso wosakayika" kuti udzakhala naco cimene upempha.” Mtima suzakhulupirira popanda kutsimikizidwa ndikuzipereka kwanu, ndi mphamvu zanu ku Mau a Mulungu. Ndicifukwa cace cikhulupiriro copanda nchito ciri cakufa. Nchito iutsa cikhulupiriro cako mucifundo ca Mulungu kwa iwe.

Cikhulupiriro ca Kristu mwa iwe cicokera kukusautsa, pamene nzeru zinai za thupi lako, monga (Kupenya, kulawa, Kuchera, kununkha, ndi Kumva) zafa, kudzera kukuleka kudya kapena kukulamulidwa. Satana alibe njira yosewenzera (ngati wa cotsedwa mwa iwe), Koma kudzera kunzeru zako zinai, kungaletse cikhulupiriro cako. Tsono popeza tikumva izi, tiyeni timange cikhulupiriro cathu pakumva mau amalonjezo ace kwa ife.

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa cosowa canu ciri conse monga mwa cuma cace m’ulemerero. Kumbukirani, kuti ngakhale thupi, ndalama, kapena za Mzimu, adzakwaniritsa zonse. “Ine ndine Mulungu amene ndikhululukira mphulupulu zako zonse, Naciritsa nthenda zako zonse.” Mudziwe kuti ananena “Zonse!” “Ndidzacotsa nthenda pakati pa iwe” (Kucotsa zonse Mu mzimu wanu).

Mulungu ndi moyo, ndi moyo wa zonse za moyo, monga maciritso, cipulumutso, cikondwelero, mtendere, ndi kulemera, zimene zili za Mzimu wamoyo ndizathupi la Kristu, thupi lace limene ndiwe. Yesu anati, “ndadza kuti akhale ndimoyo.” Kuganiza tere, ndi Mtima ndi cikhulupiriro ca Kristu, kudzera M’kumasuka kwa kumvetsa. “Kodi sadzatipatsa, Kristu, kwaulere ndi zinthu zonse,” Paulo ananena.

Mzimu wa Satana ndi imfa, m’dani wa Mulungu. Mau a Mulungu atiuza ife, kuti imfa inabwera ndi Munthu. Zooneka za imfa ndi mantha, ukali, cisoni, kubvutitsidwa, usiwa, ndi matenda. Awa onse ndi adani a Mulungu. Kristu anabwera pamulandu wa zinthu zimenezi: Mliri, nthenda yoondetsa ya cifuwa, malungo, cibayo, kutentha thupi, zirombo, cisinkwi, cinoni, nthenda yotuluka mudzi, cipere, mphere, khungu, cironda coipa cosacira naco kumaondo ndi miyendo, ndi nthenda yonse, yosalembedwa m’buku la cilamulo ici, unamasulidwa kwa iyo. Zonse zinali mtemberero lacilamulo. Muli acisomo. Kristu anali m’citenberero m’malo mwathu. Anatiombola ife kutemberero ndi thupi lace pa mtengo.

Kudwala konse ndi matenda onse odziwika, dziko lonse, anabwera cifukwa ca ucimo. Ucimo uja unali kusakhulupirira Mau a Mulungu. Hava ana cimwa ucimo uyu. Cinthu cosatuluka m’cikhulupiriro, ndico ucimo. Adamu anabweretsa anthu onse kutemberero pamulandu opanda cikhulupiriro. Kristu anaombola anthu onse kutemberero m’cikhulupiriro. Mwa Adamu, onse akufa, mwa Kristu, onse akhala ndi moyo.

Anatuma mau ace (Yesu) ndipo anaciritsidwa iwo. Cikhulupiriro m’mau ace, cicita mau kukhala thupi, tikhala mau, kalata, yodziwika ndiku werengedwa ndi anthu onse, mau a Mulungu anapangidwa thupi. Tili m’modzi ndi mau, pokhala thupi la Kristu. Mulibe matenda mwa Mulungu. Mumikwingwirima yace muna ciritsidwa.

Muli nako kuyanjana kwa Kristu. Anamulaka iye cifukwa ca mwazi wa mwana wa Nkhosa, ndi cifukwa ca mau aumboni wao, nchito ya Kalivare, mau a umboni, mukulankhula ndi macitidwe, pazimene anawacitira iwo. Musadalile mamvedwe anu, koma kukhulupirira mwa ambuye (M’mau) ndi mtima onse.

Tiyenera kubweretsa ganizo lonse kwa Kristu, kutaya zoyesa zonse, mantha, ndi kukayika, ziononga maganizo abwino, izi zidananso ndi Mulungu. Mulungu sadzaipsa mau oturuka m’milimo yake. Iye adikira mau ace kuwacita.

Ngati mumikwingwirima yace muna ciritsidwa, iye alibe sankhu la anthu, ndiponso ife tiyenera kucita zinthu zosapenyeka, kukhala ngati zopenyeka (Osakhala okhulupirira pakuona, wolungama adzakhala ndi moyo wocokera m’cikhulupiriro)" ndiko kuti, “Cikhulupiriro cako cakuciritsa.”

Mulungu atiuza m’mau ace, “Ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.” Kukhala bwino thupi lako kusungidwa ndi kulemera kwa Mzimu wako. Ndi Yehova, Mulungu wako, amene apatsa mphamvu yakuonera cuma. Muyenera kupatsa cuma canu, kunchito ya Mulungu kuti akupatseni cuma camuyaya.

Khulupirira (kumbukira, kutsutsidwa kwa Mtima) kuti matenda ako acoka zoonadi. Sichizalephera ngakhale nthawi imodzi. Munga khozeku konda matenda anu, ndiponso simungacire ndiponso muzazunzidwa, koma, ngati mukhulupirira m’coonadi, lidzasamalidwa thupi lanu, ndi kukakamizidwa, kunchito ya cilungamo ndizocitika zotsimikiza.

Mulungu sadzatisiya ngakhale kutitayaife. Mulungu salephera. Timusiya iye pa mulandu wosakhulupirira. “Pempha ndi cikhulupiriro, osakayika,” Yesu anatero. Yohane anati, “Ici ndicitsimikizo mwa iye, cimene tipempha mdzina lace tilandira.” Ngati Mtima wathu sutitsutsa, tiri nako kulimbika mtima mwa Mulungu. Paulo anati, “M’menemonso ndi ndiziyesera ndekha ndikhale naco nthawi zonse cikumbu mtima cosanditsutsa cakwa Mulungu ndi kwa anthu.” “Yense wakupempha alandira,” atero mau a Mulungu. “Ngati mudza pempha mdzina langa, ndidzacita.” Yesu anati, kuonetsa atate ace amwamba mphamvu zao. Pemphani, “Kuti cimwemwe canu cikwaniritsidwe.” Iye ananyamula nthenda zathu pa mtengo, “Ndiponso, M’mikwingwirima yace munaciritsidwa.” Yesu anati, “Kwatha.” Ngati anazitenga iye mthupi lace pa mulandu wako, tsono cifukwa ciani ukhalila nazonso, ndi cifukwa ca boza la Satana.

Kumbukira, cikhulupiriro ndi njira yoperekera maganizo ndi kufuna kwako kwa iye. Kukhulupirira mau ace, ndikukana maganizo ako ndi kulema konse ku mkwiyo. Kuganizo maganizo amalonjezo ace kudzacotsapo maganizo anu, ogonjetsa, ndiku bweretsa cikondwerero, thanzi, ndi kulemera kwainu. Ngati waleka kukhulupirira mau adzaleka kusewenza. Nthawi zonse ona maganizo ako. “Mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu.” Ganizani maganizo anu eni-eni (maganizo a Kristu) ndi kuyesa zinthu zabwino ndiponso zololedwa kwa Ambuye. Iye ndiye Mkuruwansembe, ogwiridwa ndi maganizo athu omangidwa, kupempherera ife, Mkuruwansembe wacibvomerezo cathu.

“Ndi Mtima munthu akhulupirira kutengapo cilungamo,” pamene, “m’kamwa abvomereza kutengapo cipulumutso.” Bvomereza, Khulupirira, ndi kulandila maciritso mdzina la Yesu Kristu, kucoka ku zofoka zako zonse, matenda, ndi kumagonjetso ako onse. Mulungu akudalitse ndilo pemphereo langa.

Ndine Rev. George Leon Pike Sr.

Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.

Oyera Kwa Mulungu

Uthengawu ufalitsidwa kwa ulele. Ngati mufuna kumva zambiri, lemberani ku adilesi iyi, ndipo m’mene mgugatifunire funire timabukhu iti.

CHE9908T • CHICHEWA/NYANJA • GOD’S HEALING WORD