Chikhulupiriro


Chinthu choyamba chimene ine ndikufuna kuti ndikufunseni inu omwe mukuwerenga ka traki aka ndicho, kodi ndinu Mkhristu? Mkhristu zimatanthauza kukhala monga-Khristu. Kodi inu mumachita zinthu mu moyo zomwe Khristu ankachita mu nthawi yake ya moyo? Iye ankapita kumakachita zabwino, kumakachiza onse omwe anali opsyinjika ndi mdierekezi.

Kodi cholinga chanu ndi chiani pa moyo? Ndikofunika kwambiri kuti zolinga zanu zizikhala zolondola, kapena apo chinthu chimene mukuchitacho ndi cholakwika, zilibe kanthu kuti zikuwoneka zabwino bwanji. Kodi cholinga chanu ndi chakuti mukhale ndi nyumba, kapena galimoto ndi ndalama ku banki? Kapena cholinga chanu ndi kukhala ndi bizinesi, manyado, kutchuka, kapena mphamvu mu dziko lino? Mzanga, awa ndi masomphenya osauka. Ngati inu mukanakhala munthu wolemeretsetsa, wotchuka kwambiri, ndi munthu wamphamvu kwambiri mu dziko, izo zikanangokhala zachabe ndi zosautsa mzimu. Mfumu solomoni wa m’Baibulo anali nazo zinthu zonsezi, komabe iye anadzitcha izo chabe.

Kukhala wokondedwa ndi Mulungu ndi chuma chenicheni chokhacho komanso chokhalitsa. Kukhala wophunzira kwambiri nzachabe, pakuti zonse zomwe ziri mu dziko zidzatha mkanthawi pang’ono, ndipo sipadzakhalanso kukumbukira kwa chirichonse.

Pamene ife tikuyankhula za kukonzekera tsogolo, kodi tsogololo liri kuti? Kodi ilo siliri ndi Mulungu? Mtima wa mfumu umakhala mu dzanja Lake, ndipo amautembenuzira iwo kulikonse kumene Iye akufuna chimodzimodzi monga amachitira ndi mitsinje ya madzi, Baibulo limatiuza ife. Iye amalenga zabwino, ndipo Iye amalenga zoipa, ndipo Iye ali nayo njira Yake mu zonsezo, mogwirizana ndi Malemba.

Mu dziko lino mulibemo tsogolo. Ndinkalankhula ndi mlaliki nthawi ina za tsogolo lake. Iye amakonzekera kuti azikamugwirira ntchito Mulungu akangotsiriza kugula nyumba yake, koma basi nthawi yomwe amalipira kotsiriza, mmodzi wa ana ake anamira mu nyanja kuseri kwa nyumba. Zikanakhala bwanji akanati anadzipereka kwathunthu kwa Mulungu poyamba pomwe.

Usiku wina kunabwera munthu ku misonkhano yathu, ndipo pamene Mzimu wa Mulungu unali kukokera miyoyo kuti ilape, iye anapatsidwa mwayi kuti avomereze chipulumutso, koma iye anachikana icho. Tsiku linalo pofika masana, pa mwambo wa maliro pa oyandikana nafe, ine ndinayang’ana pa nkhope yake atafa mu bokosi. Imfa inamukantha mwaliwiro iye atamukana Mulungu. Iye sanakonzekere tsogolo.

Mu msonkhano wina, ndinawapempha azibambo awiri, ndipo anakana. Posakhalitsa amuna onsewo anafa. Zingatengere malo ochuluka kuti ndifotokoze zinthu zochuluka zomwe zachitika mu utumiki wanga womwe, kutsimikizira kuti palibe tsogolo ngati palibepo Mulungu.

Woipa samakhala ndi mtendere, Baibulo limatiuza chomwecho. Mumakhala phokoso lowopsya mmakutu a wachuma lomwe silimatha. Kumazunzika ndi maganizo chifukwa cha okondedwa omwe anafa, komanso chifukwa cha matenda, misala ndi matsoka, ndi moyo wovuta.Kuyesera kulimbikira kuti usashote kapena kumuzunza mzako mwanjira ya malonda achinyengo, zimenezo si moyo. Moyo wopembedza mwachinyengo, kumadzinyenga tokha tsiku ndi tsiku mwa kulingalira kwa nzeru, kumazilimbikitsa tokha za chikhulupiriro ndi chiyembekezo zomwe mulibemo nkomwe mu mitima yathu: kodi mungati uwu ndi moyo?

Cholinga chathu chakuya chowatumikira amzathu chizikhala cholondola, ndipo tidzikhala okhudzidwa, nthawizonse kumamverera udindo wathu ngati osamalira m’bale wathu. Aliyense wa ife timadalira pa kutumikiridwa kumodzi kapena kumzake kuchokera kwa mzathu. Mulungu anaziika izi mwanjira imeneyi kuti ife tidzikhala osamalira m’bale wathu. Kaini anamupha Abele ndipo anakana kuti akhale wosamalira m’bale wake chifukwa cha zokhumba zake zachinyengo zodzikonda yekha. Mulungu adzamupatsa munthu mphoto molingana ndi ntchito zake. Iye yemwe alemera mwachinyengo adzadulidwa masiku ake asanathe, ndipo pamapeto iye adzakhala chitsiru, Malemba amatiuza chomwecho.

Musamangoganizira za manyumba abwino, zovala, ndi magalimoto zomwe mumaziwona ndi anthu. Musamangoganizira za manyado, za kutchuka ndi za maudindo amoyo zokha, koma muziganiziranso za malo azamisala, za chifuwa chachikulu, zipatala, zolemba zatsiku ndi tsiku za manyuzipepala, ndi matsoka onse a moyo, monga ngati masailini omwe amamveka pafupipafupi mmizinda. Zowopsyeza zonse izi ndi zokhumudwitsa zimandiuza ine kuti izi si zokhazo zomwe ziripo ku moyo. Alipo malo apamwamba oti nkukakhalako komwe kuli chikhalidwe cha chisangalalo, mtendere, ndi chirungamo. Kumutumikira Mulungu kumabweretsa chikhalidwe choterechi.

Liwu lochondelera lomwe lija lomwe lakhala likuitana kudutsa mzaka zana likuitanirabe pa inu ndi ine. Ilo ndi liwu la Mulungu kudzera mu utumiki ndi ana a Mulungu, kuwachondelera anthu kuyambira pomwe dziko linayamba. Liwu ili la Khristu linazikweza lokha mu mibadwo yadutsayi. Ilo linachondelera mu tsiku la Nowa chisanachitike chigumula. Ilo linachondelera mu tsiku la Khristu, matsoka aakulu asanagwere pa Yerusalemu. Ilo linayankhula ndi odzafuna malo mu mbiri yakale yoyambirira ya United States, pamene iwo ankabwera, nkumamenyana ndi mbadwa za Chimereka, pofuna kuti abisale mikuntho ya moyo. Kuchokera kale moyo umene ukumveka ndi mawu a wosungulumwa wa ku Galileya yemwe anakhala moyo wozunzika chifukwa cha inu ndi ine. Lero, liwu lomwelo likuchondelera, likupanga pempho lake lalikulu kwa dziko lamadyerero. Ine ndikufunseni inu funso ili, mzanga:chifukwa chiani ife sitikusamala kuitana uku koti ife tilape, kuti tisiye moyo wathu, ndi kuzitsitsa kukhala munthu wapansi?

Khristu anati m’badwo wotsiriza uno udzakhala wa anthu ammutu, odzikweza, ndi odzikonda okha kuposa kukonda Mulungu. Paulo anati awa ndi anthu omwe mathero a dziko adzera. Ambiri a inu omwe ine ndikuyankhula nanu munaboola kale chikumbumtima chanu ndi choboolera chamoto ndipo simukumvereranso kalikonse, chifukwa mwazipereka nokha ku mzimu wa Satana kuti muzikachita mitundu yonse ya chikunja.

Powona kuti chirichonse chidzathetsedwa kwathunthu, ndipo dziko lidzawotchedwa psyiti, Petro anafunsa, “Kodi ife tikhale anthu a mtundu wanji, tiziyankhula ndi chiyero, kuyembekezera kudza kwa tsiku la Mulungu? Petro yemweyu uyu, yemwe anapatsidwa makiyi a ufumu, anaima pa tsiku la Pentekoste, pamene mpingo unkakhazikitsidwa, ndipo anatsegula chitseko kwa mibadwo yonse. Zikwi zitatu nthawi yomweyo analowa. Mwa mabiliyoni a anthu omwe alipo pa dziko lapansi lero, ndi angati anganene kuti mawu a mtsogoleri wamkulu uyu ndi ophweka, pamene liwu la Khristu likumveka mmilomo yake, kulira kudutsa mibadwo yonse?

Kuitanirako ndikoti mulape, kuti mukabatizidwe mu dzina la Yesu Khristu kwa chikhululukiro cha machimo, kuti inu mukathe kulandira mphatso ya Mzimu Woyera, pakuti izo ndi za kwa inu ndi ana anu, ndi onse akutali, ngakhale onse omwe Ambuye, Mulungu wathu adzawaitana. Kodi inu muli pakati pa kuitana uku?

Baibulo limanena kuti anthu awa amakhala tsiku ndi tsiku, mu chiphunzitso cha atumwi. Kumbukirani, palibepo njira ina iliyonse.

Mwachisomo kudzera mu chikhulupiriro inu mumapulumutsidwa, osati mwantchito, kuwopa kuti wina angazitamandire, koma ndi mphatso ya Mulungu. Iwo anamva Mawu pamene Petro anali kulalikira, anawakhulupirira Mawu, ndipo chikhulupiriro chimene chimadza pakumva Mawu chinawonetseredwa mu miyoyo yawo mwa kumvera ku Mawu a Mulungu omwe Petro analankhula. Analandira nthawi yomweyo ubatizo wa Mzimu Woyera, Mzimu wa Mulungu wa moyo wamuyaya, chipulumutso ndi mphamvu ya chiukitsiro.

Lonjezo lomwe Mulungu anapanga kwa Abrahamu, mwa Khristu Iye analikwaniritsa pa Pentekoste, pamene Petro anati, “Lonjezo ili liri kwa onse omwe Ambuye, Mulungu wathu, adzawaitana.”

Timauzidwa kuti tizitsimikizira kuitanidwa kwathu ndi kusankhidwa kwathu. Kodi ife tingadziwe bwanji kuti ife tiri pakati pa iwo omwe anali mu kudziwidwiratu kwa Mulungu? 1 Petro 1:2 amatiuza ife kuti tinasankhidwa mogwirizana ndi kudziwidwiratu kwa Mulungu kudzera mu kuyeretsedwa kwa Mzimu kwa kumvera ndi kukonkha kwa magazi a Yesu Khristu.

Mulungu watipatsa ife zinthu zonse za moyo ndi umulungu, ndipo watiitanira ife ku ulemerero komanso ku ukoma, kwapatsidwanso kwa ife malonjezo aakulu, kuti palimodzi ndi izi ife tikakhale otenga nawo chikhalidwe chauzimu, titathawa chivundi chimene chiri mu dziko chifukwa cha kusilira. Mu ndime ya faifi, imene ikutiuza ife kuti tipereke chidwi chonse, kuti tiwonjezere ku chikhulupiriro chathu, ukoma, ndipo pa ukoma, chidziwitso, ndi pa chidziwitso, kudziletsa" ndi pa kudziletsa, chipiriro, ndi pa chipiriro, umulungu, ndi pa umulungu, chikondi cha pa abale kapena chikondi. Ngati zinthu izi zitakhala mwa inu, inu simudzakhala konse chumba kapena osabala, koma iye amene adzasowe zinthu izi iyeyo ndi wakhungu ndipo sangathe kuwona patali ndipo waiwala kuti iye anayeretsedwa ku machimo ake akale.

Chikondi chimapirira ndiponso ndi chachifundo, icho sichimaipidwa, ndipo sichimadzikonda chokha, sichimadzikweza, sichimakhala mu chikhalidwe choipa, sichimazikundikira, sichimapsyetsedwa mtima mophweka, sichimaganiza zoipa, sichimasangalala mu zoipa, koma chimasangalala mu choonadi, chimapirira zinthu zonse, chimakhulupirira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse.

Yesu anati tizidzamudziwa Mkhristu chifukwa cha zipatso zake. Ife tikudziwa kuti tinadutsa kuchokera ku imfa ndipo tinapita ku moyo chifukwa ife timawakonda abale. Mulungu ndi chikondi. Iye amene akukhala mu chikondi akukhalanso mwa Mulungu.

Zipatso za Mzimu ndi chikondi, chisangalalo, mtendere, chipiriro, kudekha, kufatsa, kudziletsa, ubwino, chikhulupiriro: pa izi palibepo lamulo. Zinthu izi zimatsimikizira kuti ndiwe woitanidwa ndi wosankhidwa ngati izo ziwonetsera mu moyo wako.

Kodi inu simukudziwa kuti wosalungama sadzalowa mu ufumu wa Mulungu? Musanyengedwe ayi" ngakhalenso aziwerewere, opembedza mafano, azigololo, olobodoka ndi zoipa, akudziipsya, akuba, awumbanda, oledzera, sadzalowa mu ufumu wa Mulungu. Paulo anati musamasocheretsane wina ndi mzake.

Muzilalikira Mawu! Mukhale osanyengerera, nthawizonse muzidzudzula, muzilimbikitsana ndi chipiriro ndi chiphunzitso. Pakuti nthawi idzafika yomwe iwo sadzamvera chiphunzitso cholamitsa, koma chifukwa cha zilakolako zawo adzaziwunjikira okha aziphunzitsi, poyabwidwa mmakutu, adzalubza pa choonadi ndipo adzapatukira kutsata nthano zachabe.

Ngati munthu wina adzaphunzitsa zosiyana ndi izi, kapena adzaphunzitsa chiphunzitso chirichonse chimene sichiri mogwirizana ndi umulungu, iyeyo ndi wodzikweza, ndi wosadziwa kanthu, wolimbana ndi mafunso obweretsa makangano. Palibe mmodzi wolungama, ayi, palibe mmodzi. Ngati nkhosa zotaika, iwo onse asochera, ndipo munthu aliyense watsata njira yake yake, ndipo Mulungu anaika pa Iye kusaweruzika kwa ife tonse. Iye anavulazidwa chifukwa cha kusaweruzika kwathu, chilango cha mtendere wathu chinaikidwa pa Iye. Ine ndikunena za chikhulupiriro chimene chinaperekedwa kamodzi kwa oyera mtima. Mukhulupirire pa Ambuye Yesu Khristu lero, ndipo mupulumutsidwe. Mulungu akudalitseni inu ndiro pemphero langa.

Zolembedwa ndi George Leon Pike Sr.

Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.

Chiyero Kwa Ambuye

Uthenga uwu umasindikizidwa kuti uzigawidwa mwaulere. Ngati mukufuna matraki ambiri chonde mulembere mu Chizungu ku adiressi ili pansipa.

CHM9915T • CHICHEWA (MALAWI) • THE FAITH