Chikhulipiro
Chinthu choyamba ndifuna kufunsa inu amene mukuwerenga uthengawu, kodi ndinu mkristu? Mkristu kutanthauza kukhala ndi moyo monga wa Yesu Kristu. Kodi m’moyo wanu mumachita zinthu zomwe Yesu Kristu anachita m’moyo wake? Anayenda-yenda nachita zabwino, nachiritsa wonse wosautsidwa ndi mdierekezi.
Kodi gwero ndi cholinga cha moyo wanu ndi chiyani? Ndichofunika kwambiri kuti cholinga chanu chikhale chabwino" kapena mukuchita chinthu cholakwika, ngakhale chikuoneka ngati ndi chabwino? Kodi cholinga chanu ndikukhala ndi nyumba, kapena kukhala ndi galimoto pamodzi ndi ndalama mu Banki, kaya mufuna kukhala ndi Bizinezi, kutamidwa, kutchuka, kapena mphamvu mu dziko lino? Bwenzi langa awa ndi masomphenya achabe. Ngati munali wolemera kwambiri, wotchukitsitsa, munthu wa mphamvu zambiri mu dziko, zonsezi ndi zachabe ndipo ndikungosautsa mzimu. Mfumu Solomoni wa m’Baibulo, anali ndi zinthu zonsezi, koma anazitcha zachabe.
Kuoneka munthu wolungama kwa Mulungu ndiye cinthu chimodzi chokondweretsa ndiponso chabwino chotifikitsa kumoyo weni-weni. Kukhala wophunzira kufika patali kulingana ndi maphunziro a masiku ano, zonsezi m’moyo wako, ziribe phindu" pakuti zinthu zonse za mdziko lino zidzaonongeka panyengo yochepa, ndiponso sikudzakhala chikumbutso cha zinthu ziri zonse za mdziko.
Ngati tinena zokonzekera za mtsogolo, nanga tsogolo ndi liti? Kodi siliri ndi Mulungu? Mulungu asunga mtima wa mfumu mdzanja lache auloza komwe afuna ngati mtsinge wa madzi, Bukhu Lopatulika litiuza. Apanga chabwino ndi choipa ndiponso njira yache ili mu zinthu zonsezi, kulingana ndi mau a Mulungu.
Kulibe za mtsogolo mdziko lino mgakhale mdziko lirinkudza, kopanda Mulungu. Ndinalankhula ndi mtsogoleri wina nthawi yina pa zamtsogolo m’moyo wache. Iye anali kuganiza zakumtumikira Mulungu atatsiriza kulipira ndalama za nyumba yache, koma pa nthawi imene analipira ndalama zache zotsiriza, mwana wache m’modzi anafera pa nyanja kuseli kwa nyumba yache. Zikanakhala bwino akanadzipereka kwa Mulungu pa chiyambi.
Munthu wina anabwera pa musonkhano wathu tsiku lina" ndipo pamene mzimu wa Mulungu unali kuyitana anthu kuti alape, munthuyo anapatsidwa nthawi yakuti alandire chipulumutso, koma anakana. M’mawa mwache pafupi nafe, m’nyumba yamaliro nthawi ya masana ndinagany’ana nkhope ya munthuyo wakufa m’bokosi. Imfa inamupeza mosachedwa atakana Mulungu. Iye sanakonzekere za kutsogolo.
Pa msonkhano wina, ndinauza amuna awiri ndiponso sanamvere. Pasanapite nthawi onse awiri anamwalira. Zingatitengere malo akuru kukamba zinthu zimene zachitira anzanga, zoonetsa kuti kulibe zamtsogolo kwaife ngati tiribe Mulungu.
Kulibe mtendere kwa oipa, Bukhu Lopatulika litiuza. Mumveka zoopsyetsa m’makutu mwa anthu wolemera zakuti sizitha kuleka. Kukhala wodwala mopitilira pa mulandu wakuopa imfa yawokondedwa, kusokezeka ndiponso kupitilira kwa mabvuto m’makhalidwe kulibe phindu. Kubvutika ndiponso kuyesa mwamphamvu kupewa mabvuto wosowa ndalama kapena kuopa kubedwa kwa katundu amene tamagwilira nchito, ndiponso kusasunga bwino anzathu munjira yopanda kumvetsa zobvuta zao, uwa siumoyo wabwino. Umoyo wodziwa mau a Mulungu koma wosatsatira, kudzinamiza ife tokha masiku wonse, pa mulandu wofuna kuganiza za m’mutu mwathu, kutsimikiza kwa ife tokha pa chikhulupiliro chosachokera m’mitima yathu. Kodi umenewu nkutchedwa umoyo wabwino?
Cholinga chathu chofikira patali panchito ya anthu anzathu chiyenera kukhala chimodzi cha zinthu zopanda bodza kapena kudzinamiza, ndiponso makhalidwe athu ayenera kukhala anzeru zabwino, masiku onse kukhala woganizira za masungidwe a abale athu. Aliyense waife ali wodalira wina ndi nzache kulingana ndi nchito zathu kwa wina ndi mzache. Mulungu anatipanga mnjira yotere" choncho ndife asungi a abale athu. Kaini anapha Abele ndiponso anakana kuti simsungi wa m’bale wache, pa mulandu wa chinyengo chache. Mulungu adzapatsa mphatso kwa munthu aliyense kulingana ndi m’mene munthuyo aliri. Iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama" pakati pa masiku ake chimdzasiya iye, ndipo pa chitsiriziro adzakhala wopusa, Mau a Mulungu atiuza motere.
Musakhale wofuna nyumba zabwino chabe, ngakhale magalimoto ndi zina zotere zimene anzanu ali nazo. Musaganize zopatsidwa ulemu, kapena kudziwika, kapenanso kukhala ndi udindo m’moyo wa dziko lino chabe, koma muganize za zipatala za anthu wofuntha (amisala) ndiponso zipatala za anthu a zifuwa, ndi zapatala za matenda wosiyana-siyana ndiponso muziwerenga nkhani za m’mapepala ndi ngozi za umoyo uno, kulingana ndi zomwe mumvera likiti-likiti m’matauni akulu monga kulira kwa chenjezo loopsya (alarm). Izi zinthu zoopsya ndiponso zonama zomwe zipatsa mantha ndi kusamvana, zindidziwatsa ine kuti uwu sindiye umoyo. Kuli m’malo m’mwamba wokhalamo komwe kuli chikondwerero, mtendere ndi chilungamo. Kumtumikira Mulungu kubwere tsa zonsezi.
Liwu lodandaulira limene lakhala likuyitana mu zaka zonse zakumbuyo, likuyitananso iwe ndi ine. Ndi liwu la Mulungu, kopyolera muntchito za Mulungu ndi ana a Mulungu, kudandaulira anthu kuchokera pachiyambi cha dziko.
Mawa awa a Yesu Kristu analankhulidwa m’mibadw yapitayi. Analankhulidwa pa nthawi ya Nowa lisanafike tsiku lachionongelo. Analankhulidwa m’masiku a Yesu Kristu pomwe ngozi isanachitike mu Yerusalemu. Anakombidwanso ku anthu amthengo, wofuna kubisala kumabvuto a moyo uno, mukupambana kwao kwabvuto m’masiku apita mumbiri ya zaka zakumbuyo. Kuchokera kale umoyo wabwino umveka ndi wa munthu wa kuGalileya amene anakhala yekha, anakhala umoyo wobvutika pa mulandu wa iwe ndi ine. Tsiku lalero liwu ili likulankhula, kulankhula kwakulu kwa anthu adziko lonse" ndikufunsa funso, “M’bale wanga, Kodi chifukwa ninji sufuna kumvera kuyitana uku kwa kuti ulape, ndi kuchoka ku makhalidwe a umoyo uyu?” Kuti uphatikane nawo wodzichepetsa.
Kristu ananena nati" m’badwo wotsiriza udzakhala waliuma, wolimbirira, wotukumuka mtima, ndiponso wokonda zokondweretsa munthu, osati wokonda Mulungu" Paulo ananena nati awa ndiwo anthu amene matsirizidwe a nthawi ya pansi pano adafika pa ife. Ambiri a inu amene ndakukambani muli kale owotchedwa ndi zisulo ku nzeru zanu ndiponso kuganiza kunatha pokhala kuti munadzipereka, kwa mzimu wa Satana, kwakuti muchita zinthu zosakondweretsa Mulungu.
Poona kuti zinthu zonse zidzaonongeka ndiponso kuti dziko lonse, lidzaotchedwa Petro anafunsa, “Kotero muyenera inu kukhala anthu wotani nanga, m’mayendedwe wopatulika m’chipembedzo,” akuyembekezera ndikufulumira kwa kudza kwache kwa tsiku la Mulungu.
Petro ameneyu anapatsidwa mfungulo za Ufumu, anayimilira pa tsiku la Pentekositi, pamene Mpingo woyamba unayambidwa ndipon anatsegula khomo ku mibadwo yonse. Anthu zikwi zitatu panthawi imeneyo anapanga khomo.
Pa awiri ndi theka kapena anthu mazana atatu amene akhala pa dziko lapansi nthawi yino, ndi angati a iwo amene adzamvera mau amtsogoleri wamkulu, pamene liwu la Ambuye Yesu limveka mkamwa mwache, kuzungulira mibadwo yonse?
Kuyitana uku ndi kwa kulapa ndi kubatizidwa mdzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo, ndiko kuti mulandira mphatso ya Mzimu woyera, pakuti lonjezano liri kwainu, ndi kwa ana anu, ndi kwa wonse akutali, wonse amene Ambuye Mulungu wathu adzayitana. Kodi ulipo pamayitanidwe amenewa?
Bukhu Lopatulika likuti anthu amenewa anali chikhalire m’chiphunzitso cha Atumwi ndi m’chiyanjano. Ukumbukire kuti palibe njira ina.
Pakuti muli wopulumutsidwa ndi chisomo chakucita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chiri mphatso ya Mulungu. Iwe unamvera kulalikira kwa Petro, ndiponso anakhulupilira mau, ndi chikhulupiliro chochokera kukumva mau a Mulungu, amene analalikidwa miniyoyo yawo, kuchokera kwa munthu wa Mulungu Petro, powalangiza kugonjera Mulungu. Pamenepo alandira ubatizo wa Mzimu woyera, Mzimu wa Mulungu wa moyo wosatha, chipulumutso ndi mphamvu yakuuka kwa kufa.
Lonjezo limene Mulungu analika kwa Abrahamu, mwa Kristu Yesu, analifikitsa pa tsiku la Pentekositi, pamene Petro ananena nati, “Ili ndilonjezano kwa inu nonse amene Mulungu Ambuye wathu adzayitana.”
Tikuuzidwa kuti tipange maitanidwa athu ndi masankhulidwe athu m’choonadi. Kodi tingadziwe bwanji kuti tiri amodzi a anthu amene anasankhidwa ndi Mulungu? I Petro 1:2 akutiuza ndife wosankhidwa, kulingana ndi masankhulidwe a Mulungu, kudzera mukuyeretsa kwa Mzimu, ndikugonjera ndi kusambitsa kwa mwazi wa Ambuye Yesu Kristu.
Mulungu anatipatsa ife zinthu zimene zipereka kumoyo ndi makhalidwe womukondweretsa Iye, ndiponso adatiitana ife ndi ulemerero ndi kukoma kwache kwa Iye yekha. Mwa izi anatipatsa malonjezano a mtengo wache ndi akuru ndithu" kuti mwa izi mukakhale woyanjana nawo Umulungu wache, mutapulumuka ku chibvundi chiri pa dziko lapansi m’chilako-lako.
Ndime ya chisanu itiuza ife kuti, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi pa ukoma chizindikiritso chodziletsa" ndipachodziletsa chipiriro" ndi pa chipiriro chipembedzo" ndi pa chipembedzo chikondi cha pa abale" ndi chikondi cha pa abale chikendi. Pakuti izi zikakhala ndi inu, ndipo zikachuruka zidzachita kuti musakhale aulesi" pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, wa chimbuuzi, woyiwala matsukidwe ache potaya zoyipa zache zakale.
Chikondi chikhale chilezere, chiri chokoma mtima" chikondi sichidukidwa" chikondi sichidziwa kuzitamanda, sichidzikuza, sichichita, zosayenera, sichitsata za mwini yekha sichipsya mtima, sichilingilira zoipa" sichikondwera ndi chiyengo, koma chikondwera ndi choonadi" chikwiria zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Yesu ananena nati, muzadziwa mkristu molingana ndi zomwe achita. Tidziwa tachoka ku imfa kulowa m’moyo, pa mulandu wa chikondi chathu kwa abale. Mulungu ndi chikondi. Amene ali mchikendi, ali mwa Mulungu.
Chipatso cha Mzium ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso" pokana zimenezi palibe lamulo. Izi zinthu zingalangize kuti ndiwe m’modzi wa anthu wosankhidwa, ngati zioneka m’moyo wako.
Kapena sudziwa kuti wosalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe" adama, kapena wopembedza mafano, kapena achigololo, kapena wolobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsya ndi amuna, kapena ambala, kapena wosiria, kapena woledzera, kapena wolalatira, kapen wolanda, sadzalowa ufumu was Mulungu. Paulo ananena nati, musadzisocheretse inu nokha.
Lalikira mau" chita nawo pa nthawi yache, popanda nthawi yache, tsutsa, dzudzula, chenjeza, ndikuleza mtima konse ndi chiphunzitso. Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa" komatu poyabwa mkhutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwazilako-lako za iwo wokha: ndipo adzalubza dala pa choonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zachabe.
Ngati munthu wina aphunzitsa maphunzitso ena, wosalingana ndi awa, kapena maphunzitso amene sakandweretsa Mulungu" kapena munthu anyada, ndiponso wosadziwa kanthu, koma kufunsa-funsa mafunso, ndiko kuti adzaononga ntchito yonse pamulandu wa zolakwa zache. Palibe m’modzi wolungama, inde palibe m’modzi. Ngati nkhosa zotayika, munthu aliyense kwa iye yekha" koma Mulungu anayika pa Iye, zolakwa zaife tonse. Anatundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu" chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera iye. Ndikamba zachikhulupiriro, chimene chinapatsidwa kwa wokhulupirira" khulupirira mwa Ambuye Yesu Kristu lero lomwe ndi kupulumutsidwa. Mulungu akudalitse, ili ndilo pemphero langa.
Ndine Rev. George Leon Pike Sr.
Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.
Oyera Kwa Mulungu
Kapepala ka Uthenga aka kafalitsidwa kuti kadzipelekedwa kwaulele. Ngati mukufuna timapepala ta Uthenga tina, lembelani kalata ku adiresi ili mmunsimu ngati kungatheke mulembe m’Chingerezi, munene mufuna angati amene inu mungagwirire ntchito.
CHE9915T • CHICHEWA/NYANJA • THE FAITH