Chivumbulutso Choonadi
Ine ndifuna kukamba nanu chinthu china chimene chiri chofunika m’moyo wa munthu kapena m’chikhalidwe chokhudzana ndi chipulumutso. Phunziro lake ndi lokhuzana ndi kudzadzidwa ndi mzimu woyera ndi kufunika kwake kwa ubatizo.
Ife tidzindikire kuti tiri pansi pa mzere osonyeza chikhalidwe cha bwino pa chipangano chofunika chimene tinaimirira patsogolo pa madzi a ubatizo.
Ndiye njira ya bwino ya phunziroli yafotokozedwa mu chaputala chachiwiri cha uthenga wabwino wa machitidwe, m’menemo mulungu ali kuonetsa ntchito zake za phunziroli.
Mtumwi Peturo atasankhidwa ndi mulungu kukatsegula khomo la kumwamba kwa onse ana a Isaraeli ndi anthu wamba anaonetsa mphavu pamene akalimbana kugonjetsa mphavu yo ufumu wa satana, polalikira kwa anthu kuti amvetse kuti kulapa, ubatizo ndi kudzadzidwa ndi mzimu woyera ndiyo njira yoyenera ya kwa mulungu. Iye anawalamulira izi m’njira ya chikristu.
Ena adzakusogolerani inu kuti mukhulu pirire kuti kudzadzidwa ndi mzimu woyera sichinthu chofunikira ku njira ya chipulumutso. Iwo amakhulupirira kuti choyenera kuchita ndi kukhala ndi cholinga. Koma Paulo anati mukakhala ndi cholinga mudzichione tsera.
Ndiye choncho pali njira zitatu za ubatizo zimene Paulo ayerekeza ngati ulaliki wa ubatizo. Njira zimenezi zikhala ngati mutu wa mulungu. Uku ndiye kuti ali atatu mwa m’modzi, mulungu, mzimu woyera, ndi mulungu mwana monga pachiyambi cha umunthu. M’mene chikhalira, m’mene ife tidziwira kuti mulungu mwini alibe chiyambi, popeza iye anali, ndipo ali wachikhalire ali kudziwika kwa ife ngati mulungu atate. Wopambana mu uzimu, ndipo ali wachikhalire kuyambira pa chiyambi.
Atapita iye, monga mau ake atsandulika atsopano kapena m’mene tikhoza kunenera mwa umunthu, anadzitsimikizira iye mwini mwa Kristu Yesu, ife tidzindikira iye mu ndime yachiwiri ya nyumba yake ngati mwana wa mulungu.
Chinthu chichitatu chimene tifuna kunena pano m’mau ake a mulungu ndi ichi, m’bado uno wachitatu wa mulungu, mulungu ali kudziwika ngati mzimu woyera, choncho nsaru itabwerekedwa, kapena thupi la munthu litaukitsidwa m’manda, nalitseguka pa mtanda, ndikuyenda kwa udzimu wa umunthu umene unaonekera mu chifanizo chake kukhala ngati m’mene munthu adzindikira chinthu.
Maganizo athu eni-eni amene alibe malire ndi mulungu, ali omveka kwa amene ali chitsanzo chabwino cha uzimu kusiyana ndi amene saali chitsanzo chabwino cha Yesu Khristu.
Tsopano tikudziwa m’mene mulungu chilili, ndimakhalidwe ake, ndi chifundo chake chosatha m’mene chilili pa ife anthu, ndipo tiri omvetsetsa mwa mulungu kudzera mwa mwana wake Yesu Khristu.
Ndiye tsopano tikuona chifukwa chake chimene munthu ayenera kubatizidwa mu dzina la Yesu Khristu. M’bukhu lopatulika mwanenedwa kuti palibe dzina lina lopasidwa kumwamba kapena pakati pa anthu, limene liri ndi chipulumutso, limene tinga pulumutsidwe nalo, m’mabukhuonse a mulungu monga mwamachitidwe a tumwi anena, koma m’kalata imodzi, onse ali kuonana maso ndi maso kunena zimodzi modzi kupitiriza chisimikizo mu uthenga wabwino wa apositoli.
Ngakhale mu bukhu la machitidwe pa chaputala 8 m’mene Filipo ali kulalikira kapena pa chaputala 10 pamene Peturo ali kulalikira, kapenanso mu chaputala la 19 m’mene Paulo ali kulalikira, tiri kuona kuti onse ali kutsimikiza dzina la Yesu pokhudzana ndi ubatizo ngati njira yopita ku ufumu wa mulungu.
Chifukwa chake cha ubatizo ndi choti ife timabatizidwa mu imfa yake, tiri kudzalidwamwa iye tonse mwa chifanizo cha imfa yake.
Choncho kudzera mu dzina lake la ule me lero, tadzutsidwa ife tonse m’chifanizo cha kuuka kwake kwa akufa, choncho titakhala mwa Yesu, ndiye kuti tapulumuka mu uchimo wa Adamu ndi kuti tsopano takwatiwa kwa ena ngakhale kwa Yesu wa moyo. Tsopano kwa Paulo tikhoza kunena kuti, siine amene ali ndi moyo koma Khristu amene akhala ndi ine, ndi moyo umene ine ndiri nao lero, ndikhalira dzina la mwana wa mulungu.
Tsopano tiri kuona kuti chikhulupiriro cha ubatizo monga m’mene chaneneredwa m’mabukhu a mulungu kuti choyamba ndi madzi amene ayankha za chigumula cha nthawi ya Nowa, kapena zigawo za thupi, madzi ndiye moyo wazomera zonse, chachiwiri ndi mwazi umene uli moyo wa munthu ali yense umene munthu walandira ngati kwa sing’anga potchinjiriza moyo wake. Chinthu ichi, zoonadi chiyankha mwazi wa pamtanda.
Chachitatu tiri ndi mzimu umene ukanapungulidwa pa thupi lathu masiku omaliza, achisangalalo. Ichi ndi chinthu chimene china patsidwa kwa chalichi. Ife tikutsimikizira izi m’maganizo athu eni-eni, poganizira za kulandira kwathu kwa uzimu.
Ndiye sopanotiri kuona madzi, mwazi ndi mzimu, chimodzi ku thupi, chimodzi ku mzimu ndi chimodzi ku nzeru. Ntchito zitatuzi zipangitsa ife kukhala antunthu mwa iye, tinalengedwanso muchifaniziro chake ndi mphavu ya mulungu (thupi, mzimu ndi nzeru monga ngati zinthu zitatu mwa chimodzi, zimene ziri Atate, mwana ndi mzimu). Monga amatiuzira malembo oyera kuti zinthu zitatuzi ndi chimodzi.
Pomaliza pa zinthu zimene tanena, ngakhale ife tiri odzindikira kuti zonse za mau a mulungu zimatitumikira ndiku titsogolera pa moyo wathu wazofuna za umunthu. Komabe mukuphunzira ndi kufufuza-fufuza kwathu tapezamo choonadi. Ponena zoona, chipangano cha kale ndi malamulo ake chikuimiria ana a Isalaeri, (madzi, dziko ndi zomera) zimene ziimiria nyengo ya utate. Chipangano chatsopano ndi chifundo chake ziimiria anthu wamba (dziko la mwazi), umene. Uonetsa umwana. Chipangano cha uzimu chimene chiri mbukhu la chibvumbulutso ndi chibvu mbulutso chake choonadi kapena chikondi cha mulungu, chimene chiimirira mpingo woyera wa mulungu (kapena dziko la angelo) imenenso ndi nyengo ya mzimu woyera. Nyengo yoyamba imasonyeza atate, nyengo yachiwiri isonyeza amayi (kuwawidwa kwa kalivari) kachitatu tiri ana a mulungu.
Ndine Rev. George Leon Pike Sr.
Founder and first President of Jesus Christ’s Eternal Kingdom of Abundant Life, Inc.
Woyera Kwa Mulungu
Uthengawu wadindidwa kuti ugawidwe kwa ulele. Ngati mufuna kulandira zambiri, mutha kulembera ku adilesi ili musiyi, ndipo mutiuze matraki angati mungawagwiritse ntchito mwa nzeru.
CHE9913T • CHICHEWA/NYANJA • REVELATIONAL TRUTHS